Masalimo 69:29 - Buku Lopatulika Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine ndazunzika ndipo ndikumva kuŵaŵa. Nyamuleni Inu Mulungu, kuti ndipulumuke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikumva zowawa ndi kuzunzika; lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.
Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.
Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa.
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.