Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
Masalimo 69:23 - Buku Lopatulika M'maso mwao mude, kuti asapenye; ndipo munjenjemeretse m'chuuno mwao kosalekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'maso mwao mude, kuti asapenye; ndipo munjenjemeretse m'chuuno mwao kosalekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maso ao achite chidima kuti asathe kupenya, ziwuno zao zizinjenjemera kosalekeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale. |
Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.