Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
Masalimo 69:22 - Buku Lopatulika Gome lao likhale msampha pamaso pao; pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Gome lao likhale msampha pamaso pao; pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zakudya zao zisanduke msampha. Akodwe ndi maphwando a nsembe zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha; chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe. |
Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.