Masalimo 69:20 - Buku Lopatulika Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wanga wasweka chifukwa cha zipongwe, ndataya mtima kotheratu. Ndidafunafuna ena ondichitira chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe. Ndidafunafunanso ena ondisangalatsa, koma sindidampeze ndi mmodzi yemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe. |
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine.
Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?
Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.
Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,
kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;