Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.
Masalimo 69:17 - Buku Lopatulika Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu, fulumirani kundithandiza, pakuti ndili pa zovuta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto. |
Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.
Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.
Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?