Masalimo 69:16 - Buku Lopatulika Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino. Munditchere khutu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine. |
Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.
Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.