Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.
Masalimo 69:15 - Buku Lopatulika Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musalole kuti chigumula chindikokolole, kapena kuti nyanja yakuya indimize. Musalole kuti manda atseke kukamwa atandimeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musalole kuti chigumula chindimeze, kuya kusandimeze ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza. |
Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.
pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.
yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.
iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.