Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.
Masalimo 69:14 - Buku Lopatulika Mundilanditse kuthope, ndisamiremo, ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundilanditse kuthope, ndisamiremo, ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni kuti ndisamire m'matope, landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mundilanditse kuchoka mʼmatope, musalole kuti ndimire, pulumutseni ine kwa iwo amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama. |
Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.
Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba; ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu, kudzanja la alendo;
Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.
Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?
Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.