pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
Masalimo 69:11 - Buku Lopatulika Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pomwe ndavala chiguduli, anthu amandiseweretsa. |
pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
Anandiyesanso chitonzo cha anthu; ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake.
Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.
Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;
Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
Lirani ngati namwali wodzimangira m'chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.
Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.