Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.
Masalimo 68:1 - Buku Lopatulika Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane; adani ake athawe pamaso pake. |
Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.
Musawapheretu, angaiwale anthu anga, muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse, Ambuye, ndinu chikopa chathu.
Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala mu Zalimoni.
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.
Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.
Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, ndipo zinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.
Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.