Masalimo 66:8 - Buku Lopatulika Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lemekezani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthunu, mau omtamanda Iye amveke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke; |
Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza.
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.
Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.
Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;