Masalimo 66:6 - Buku Lopatulika Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma. Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi. Nchifukwa chake timukondwerere Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye. |
Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.
Ndipo kunali pochoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordani, ansembe anasenza likasa la chipangano pamaso pa anthu.
pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.
Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.