Masalimo 66:5 - Buku Lopatulika Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu. |
Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.
Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.
Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.
Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.