Masalimo 66:16 - Buku Lopatulika Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira. |
Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire mu Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.
Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.
chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;