Masalimo 66:13 - Buku Lopatulika Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga. |
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.
Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.
Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.
Mukalowa m'munda wampesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m'chotengera chanu.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.