Masalimo 66:11 - Buku Lopatulika Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu. |
Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.
Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.
Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.
Dalitsani, Yehova, mphamvu yake, nimulandire ntchito ya manja ake; akantheni m'chuuno iwo akumuukira, ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.