Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.
Masalimo 65:2 - Buku Lopatulika Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu amene mumamvera pemphero, anthu onse adzabwera kwa Inu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika. |
Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.
Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.
Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu mu ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.
Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.
nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.
Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.