Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 64:9 - Buku Lopatulika

Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pompo anthu onse adzachita mantha, adzasimba zimene Mulungu wachita, adzalingalira zomwe Mulungu wachitazo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anthu onse adzachita mantha; adzalengeza ntchito za Mulungu ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.

Onani mutuwo



Masalimo 64:9
13 Mawu Ofanana  

Mtima wanga wasweka ndi kukhumba maweruzo anu nyengo zonse.


Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.


Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.


Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi.


Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.


Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire mu Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.


Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichite kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.