Masalimo 64:2 - Buku Lopatulika Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa, ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa. |
Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.
Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.
nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.