Masalimo 64:1 - Buku Lopatulika Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imvani Yehova, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Imvani mau anga, Inu Mulungu, pamene ndikukudandaulirani. Tetezani moyo wanga kwa mdani woopsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga; tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani. |
Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.
nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.