Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 61:8 - Buku Lopatulika

Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero nthaŵi zonse ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, tsiku ndi tsiku ndidzachitadi zimene ndidalumbirazo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo



Masalimo 61:8
10 Mawu Ofanana  

Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe.


Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.


kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.


Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.


Mu Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu, adzakuchitirani Inu chowindachi.


Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa, kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga; ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze, ndinu Woyerayo wa Israele.


Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.


Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.