Masalimo 61:5 - Buku Lopatulika Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, mwamva zimene ndalumbira popemphera. Inu mwandipatsa choloŵa chimene amalandira anthu oopa dzina lanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga; mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu. |
Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.