Masalimo 61:1 - Buku Lopatulika Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa. |
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.