Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Masalimo 60:8 - Buku Lopatulika Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine. Edomu adzakhala poponda nsapato zanga. Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.” |
Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.
Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Ndipo anaika asilikali a boma mu Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu.