Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 60:7 - Buku Lopatulika

Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga. Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera, Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu

Onani mutuwo



Masalimo 60:7
9 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.


Ndi tsidya lija la Yordani a Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, ndi zina zilizonse za khamu kuchita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri.


Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera: ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.


Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani.


Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.