Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
Masalimo 60:4 - Buku Lopatulika Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Inu mwatikwezera mbendera ife amene timakuwopani, kuti tisonkhanireko pothaŵa uta wankhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta. |
Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.
Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akulu.
Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako aamuna pa chifuwa chao, ndi ana ako aakazi adzatengedwa pa mapewa ao.
Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga;
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.