Masalimo 59:9 - Buku Lopatulika Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mphamvu zanga, maso anga ali pa Inu, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa. |
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa chifundo changa.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.
Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga.