Masalimo 59:7 - Buku Lopatulika Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Awo ali ukowo, akulongolola kwambiri, ndipo akufuula mwankhalwe, chifukwa m'maganizo mwao amati, “Ndani akutimva nanga?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo; iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo, ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?” |
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.
Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.
Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.
Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.