Masalimo 59:2 - Buku Lopatulika Mundilanditse kwa ochita zopanda pake, ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundilanditse kwa ochita zopanda pake, ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni kwa anthu ochita zoipa, landitseni kwa anthu okhetsa magazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi. |
Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;
Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?