Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
Masalimo 59:13 - Buku Lopatulika Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo. |
Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya.
Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.
Musawapheretu, angaiwale anthu anga, muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse, Ambuye, ndinu chikopa chathu.
Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele.
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova.