Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Masalimo 59:1 - Buku Lopatulika Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga, ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga, ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pulumutseni kwa adani anga, Inu Mulungu wanga, tetezeni kwa anthu ondiwukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu; munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane. |
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.
Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.
Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.
Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?
Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa, m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.