Masalimo 58:2 - Buku Lopatulika Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde, mumtima muchita zosalungama; pa dziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyai, mitima yanu imangolingalira zoipa, kuweruza kwanu kosalungama kumadzetsa chiwawa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi. |
Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.
Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.
Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.
Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.