Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Masalimo 57:9 - Buku Lopatulika Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a maiko onse, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko. |
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.
Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.