Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.
Masalimo 57:8 - Buku Lopatulika Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lumpha iwe mtima wanga. Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani, Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuka moyo wanga! Dzukani zeze ndi pangwe! Ndidzadzuka mʼbandakucha. |
Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.
Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.
Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.
mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo.
Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.