Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Masalimo 57:2 - Buku Lopatulika Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; ndiye Mulungu wonditsirizira zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; ndiye Mulungu wonditsirizira zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulirira Mulungu Wopambanazonse, Mulungu amene amandichitiradi zonse zimene walonjeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba, kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine. |
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.