Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
Masalimo 57:10 - Buku Lopatulika Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba; kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo. |
Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.
Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa chifundo changa.
Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zazikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?