Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.
Masalimo 56:3 - Buku Lopatulika Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikachita mantha ndimadalira Inu. |
Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.
Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.