Masalimo 56:2 - Buku Lopatulika Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adani akundizunza tsiku lonse, pali ambiri amene akumenyana nane monyada. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada. |
Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;
Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi?
pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.