Masalimo 55:4 - Buku Lopatulika Mtima wanga uwawa m'kati mwanga; ndipo zoopsa za imfa zandigwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtima wanga uwawa m'kati mwanga; ndipo zoopsa za imfa zandigwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wanga ukumva ululu woopsa, zoopsa za imfa zandigwera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga; mantha a imfa andigwera. |
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.
Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,