Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Masalimo 55:2 - Buku Lopatulika Mverani, ndipo mundiyankhe, ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mverani, ndipo mundiyankhe, ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundimvere, ndipo mundiyankhe. Mtima wanga suli m'malo chifukwa cha mavuto anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mverani ndipo mundiyankhe. Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru |
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?
Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.
Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.