Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Masalimo 55:1 - Buku Lopatulika Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu; ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu; ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, tcherani khutu kuti mumve pemphero langa, musabisale pamene ndikukupembani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu, musakufulatire kupempha kwanga, |
Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.