Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Masalimo 54:3 - Buku Lopatulika Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onyada andiwukira, anthu ankhalwe amafunafuna moyo wanga, iwo saganizako za Inu Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu. |
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.
Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Kodi ochita zopanda pake sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; ndipo saitana Mulungu.
Mulungu, odzikuza andiukira, ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga, ndipo sanaike Inu pamaso pao.