Masalimo 53:5 - Buku Lopatulika Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse. Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani. Inu mudzaŵachititsa manyazi chifukwa Mulungu waŵakana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza. |
Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.
Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.
Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.
Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata mu Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.
Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.