Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira.