Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.
Masalimo 52:9 - Buku Lopatulika Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya, chifukwa cha zimene mwachita. Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani, pakuti ndinu abwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu. |
Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.
Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.