M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
Masalimo 52:1 - Buku Lopatulika Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwanji ukunyadira ntchito zako zoipa, munthu wamphamvuwe? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu? |
M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.
Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.