Masalimo 51:7 - Buku Lopatulika Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera, munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala |
Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;