Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
Masalimo 51:5 - Buku Lopatulika Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo, ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga adatenga pathupi pa ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa, wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine. |
Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.
Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;