Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.
Masalimo 51:10 - Buku Lopatulika Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine. |
Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.
Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?
Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.
ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse.
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;