Sindidzatenga ng'ombe m'nyumba mwako, kapena mbuzi m'makola mwako.
Ndithudi, sindilandira ng'ombe kapena mbuzi iliyonse ya m'makola anu.
Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako kapena mbuzi za mʼkhola lako,
Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine,
Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda.
satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;